Jeremiah 2:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zovala zanu zili psu ndi magazi a anthu osauka osachimwa. Anthuwo simudaŵapeze nathyola nyumba. Komabe, ngakhale zinthu zili choncho,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso m'nsalu zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osachimwa; sunawapeza pakuboola, koma ponsepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale pa zovala zako anthu amapezapo magazi a anthu osauka osalakwa. Anthuwo simunawapeze akuthyola nyumba. Komabe ngakhale zinthu zili chomwechi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso m'nsaru zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osacimwa; sunawapeza pakuboola, koma ponsepo.