Jeremiah 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sadalabadeko za Ine Chauta, ngakhale ndine amene ndidaŵatulutsa m'dziko la Aejipito, ndi kuŵatsogolera m'chipululu, m'dziko louma ndi lokumbikakumbika, m'dziko lachilala ndi la mdima wandiweyani, m'dziko limene munthu sadutsamo, kumene sikukhala munthu konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Osati Ali kuti Yehova amene anatikweza kuchokera kudziko la Ejipito, natitsogolera m'chipululu, m'dziko loti see ndi la maenje, m'dziko la chilala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitanso anthu, losamangamo anthu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo sanafunse nʼkomwe kuti, ‘Kodi Yehova ali kuti, amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto natitsogolera mʼchipululu mʼdziko lowuma ndi lokumbikakumbika, mʼdziko lopanda mvula ndi la mdima, dziko limene munthu sadutsamo ndipo simukhala munthu aliyense?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Osati, Ali kuti Yehova amene anatikweza kucokera ku dziko la Aigupto, natitsogolera m'cipululu, m'dziko loti se ndi la maenje, m'dziko la cirala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitamo anthu, losamangamo anthu?