Jeremiah 20:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndimamva ambiri akunong'ona. Zoopsa zili pa mbali zonse! Amati, “Kamnenezeni! Tiyeni tikamneneze!” Amene adaali abwenzi anga amayembekeza kuti ndigwa pansi, amati, “Mwina mwake adzatha kunyengedwa, tsono ife tidzamgwira ndi kulipsira pa iyeyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzamlaka iye, ndipo tidzambwezera chilango.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndimamva anthu ambiri akunongʼona kuti, “Zoopsa ku mbali zonse! Kamunenezeni! Tiyeni tikamuneneze!” Onse amene anali abwenzi anga akuyembekezera kuti ndigwa pansi, akumanena kuti, “Mwina mwake adzanyengedwa; tidzamugwira ndi kulipsira pa iye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzamlaka iye, ndipo tidzambwezera cilango.