Jeremiah 20:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta ali nane, ndiye wankhondo woopsa. Nchifukwa chake anthu ondizunza adzakhumudwa, ndithu sadzandipambana. Adzachita manyazi kwambiri, chifukwa cha kundilepherako, ndipo manyazi aowo sadzaiŵalika konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsa; chifukwa chake ondisautsa adzaphunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, chifukwa sanachite chanzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova ali nane, ndiye wankhondo wamphamvu. Nʼchifukwa chake ondizunza adzalephera ndipo sadzandipambana. Adzachita manyazi kwambiri chifukwa sadzapambana. Manyazi awo sadzayiwalika konse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Yehova ali ndi ine ngati wamphamvu ndi woopsya; cifukwa cace ondisautsa adzapunthwa, sadzandilala; adzakhala ndi manyazi ambiri, cifukwa sanacita canzeru, ngakhale ndi kunyazitsa kwamuyaya kumene sikudzaiwalika.