Jeremiah 20:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta Wamphamvuzonse, amene mumaweruza anthu molungama, amene mumapenya zamumtima, ndikupereka mlandu wanga kwa Inu. Ndikukupemphani kuti mundilipsirire adani anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma, Inu Yehova wa makamu, amene muyesa olungama, amene muona impso ndi mtima, mundionetse ine kubwezera chilango kwanu pa iwo; pakuti kwa inu ndaululira mlandu wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumayesa anthu molungama ndipo mupenya za mu mtima mwa munthu. Ndiloleni kuti ndione kuti mwalipsira adani anga popeza ndapereka mlandu wanga kwa Inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma, Inu Yehova wa makamu, amene muyesa olungama, amene muona imso ndi mtima, mundionetse ine kubwezera cilango kwanu pa iwo; pakuti kwa inu ndaululira mlandu wanga.