Jeremiah 20:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Chauta akunena kuti: Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe, ndiponso kwa abwenzi ako onse. Abwenzi akowo adani ao adzaŵapha ndi lupanga, iweyo ukupenya. Ndipo Yuda yense ndidzampereka kwa mfumu ya ku Babiloni. Ena adzaŵatenga ukapolo kupita nawo ku Babiloni, ndipo ena adzaŵapha ndi lupanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe choopsa cha kwa iwe mwini, ndi kwa abwenzi ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzawatengera iwo am'nsinga ku Babiloni, nadzawapha ndi lupanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yehova akuti, ‘Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe ndi kwa abwenzi ako onse; iweyo ukuona. Anthu a ku Yuda ndidzawapereka onse mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ena adzatengedwa ukapolo ku Babuloni ndipo ena adzaphedwa pa nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova atero, Taonani, ndidzakuyesa iwe coopsa ca kwa iwe mwini, ndi kwa abale ako onse; ndipo iwo adzagwa ndi lupanga la adani ao, ndipo maso ako adzaona; ndipo ndidzapereka Ayuda onse m'dzanja la mfumu ya ku Babulo, ndipo iye adzawatengera iwo am'nsinga ku Babulo, nadzawapha ndi lupanga,