Jeremiah 20:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chuma chonse chamumzindamu, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zonse za mtengo wapatali ndi chuma cha mafumu a ku Yuda, zonsezo ndidzazipereka kwa adani ao. Iwowo adzafunkha zimenezi ndi kupita nazo ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso ndidzapereka chuma chonse cha mudzi uwu, ndi zaphindu zake zonse, ndi zinthu zake zonse za mtengo wake, inde, zolemera zonse za mafumu a Yuda ndidzapereka m'manja mwa adani ao, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzapereka kwa adani awo chuma chonse cha mu mzinda uno, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zake zonse za mtengowapatali ndiponso katundu yense wa mafumu a ku Yuda. Iwo adzazitenga monga zinthu zolanda ku nkhondo ndi kupita nazo ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso ndidzapereka cuma conse ca mudzi uwu, ndi zaphindu zace zonse, ndi zinthu zace zonse za mtengo wace, inde, zolemera zonse za mafumu a Yuda ndidzapereka m'manja mwa adani ao, amene adzazifunkha, nadzazitenga kunka nazo ku Babulo.