Jeremiah 20:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, mwandipusitsa ine, ndipo ndapusadi. Inu ndinu amphamvu kuposa ine, ndipo mwandipambana. Aliyense akundiseka tsiku lonse, aliyense akundinyodola kosalekeza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwalakika; ine ndikhala choseketsa dzuwa lonse, onse andiseka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova, mwandinamiza, ndipo ndinapusadi; Inu ndi wamphamvu kuposa ine ndipo munandipambana. Anthu akundinyoza tsiku lonse. Aliyense akundiseka kosalekeza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwalakika; ine ndikhala coseketsa dzuwa lonse, lonse andiseka.