Jeremiah 20:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikanena kuti, “Sindidzalalikanso za Chauta, sindidzalankhulanso m'dzina lake,” mau anu, Inu Chauta, amayaka ngati moto mumtima mwanga. Ndimayesa kuŵasunga m'kati, koma pambuyo pake ndimaŵatulutsa popeza kuti sindingathe kupirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndikanena kuti, “Sindidzalalikiranso za Iye kapena kuyankhulanso mʼdzina lake,” mawu anu amayaka ngati moto mu mtima mwanga, amakhaladi ngati moto wotsekeredwa mʼmafupa anga. Ndapirira kusunga mawu anu mu mtima mwanga osawatulutsa, koma sindingathe kupirirabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati nditi, Sindidzamchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lace, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.