Jeremiah 21:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu a m'banja la Davide, Chauta akunena kuti: “ ‘Muziweruza motsata chilungamo m'maŵa mulimonse, ndipo muzipulumutsa kwa anthu ozunza, aliyense amene katundu wake wabedwa, kuwopa kuti mkwiyo wanga ungayake nkukhala wosazimika, chifukwa cha machimo anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nyumba ya Davide iwe, Yehova atero, Chita chiweruzo m'mawa, ndi kumlanditsa amene afunkhidwa m'dzanja la wosautsa, kungatuluke kupsa mtima kwanga ngati moto, ndi kutentha kosazimika, chifukwa cha ntchito zanu zoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
inu a mʼbanja la Davide, Yehova akuti, “ ‘Weruzani mwachilungamo mmawa uliwonse; pulumutsani mʼdzanja la wozunza aliyense amene walandidwa katundu wake, kuopa kuti ukali wanga ungabuke ndi kuyaka ngati moto wosazimitsika chifukwa cha zoyipa zimene mwachita.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nyumba ya Davide iwe, Yehova atero, Cita ciweruzo m'mawa, ndi kumlanditsa amene afunkhidwa m'dzanja la wosautsa, kungaturuke kupsa mtima kwanga ngati moto, ndi kutentha kosazimika, cifukwa ca nchito zanu zoipa,