Jeremiah 21:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“ ‘Ndikukuimbani mlandu, inu anthu okhala m'chigwa inu okhala ngati thanthwe lapachidikha,’ ” akutero Chauta. “Inu amene mumati, ‘Ndani angatithire nkhondo? Ndani angathe kuloŵa m'malinga mwathu?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'chigwa, ndi pa thanthwe la m'chidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? Ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzalimbana nanu, inu amene mukukhala pamwamba pa chigwa, inu okhala ngati thanthwe lapachidikha, akutero Yehova. Inu amene mumanena kuti, ‘Ndani amene angabwere kudzalimbana nafe? Ndani amene angathe kulowa mʼmalinga mwathu?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, Ine ndine mdani wako, iwe wokhala m'cigwa, ndi pa thanthwe la m'cidikha, ati Yehova; inu amene muti, Ndani adzatsikira kumenyana ndi ife? ndani adzalowa m'zokhalamo zathu?