Jeremiah 21:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pitani kwa Yeremiya mukampemphe kuti atinenere kwa Chauta, popeza kuti Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni akufuna kutithira nkhondo. Mwina mwake Chauta nkutichitira zodabwitsa, kuti Nebukadinezara achoke kwathu kuno.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tifunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadinezara mfumu wa ku Babiloni atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzatichitira ife monga mwa ntchito zake zolapitsa, kuti atichokere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo amati akanene kwa Yeremiya mawu akuti, “Tinenere kwa Yehova chifukwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni akutithira nkhondo. Mwina mwake Yehova nʼkutichitira zodabwitsa kuti Nebukadinezarayo achoke kwathu kuno.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Titunsirenitu ife kwa Yehova; pakuti Nebukadirezara mfumu wa ku Babulo atithira ife nkhondo; kapena Yehova adzaticitira ife monga mwa nchito zace zolapitsa, kuti aticokere.