Jeremiah 21:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mukamuuze Zedekiya kuti Chauta, Mulungu wa Israele akuti, ‘Ndidzakulandani zida zankhondo zimene zili m'manja mwanuzo, zimene mukumenya nazo nkhondo ndi mfumu ya ku Babiloni ndi ankhondo ake amene akuzingani ndi zithando zankhondo. Ndidzabwera nazo ndi kuziika m'kati mwa mzinda uno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova, Mulungu wa Israele atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene zili m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babiloni, ndi Ababiloni akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mudzi uwu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ndikulandeni zida zimene zili mʼmanja mwanu zimene mukugwiritsa ntchito polimbana ndi mfumu ya ku Babuloni ndi ankhondo ake amene akuzingani kunja kwa lingali. Ndipo ndidzasonkhanitsa zidazo mʼkati mwa mzindawu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova, Mulungu wa Israyeli atero, Taonani, ndidzabweza zida za nkhondo zimene ziri m'manja anu, zimene mumenyana nazo ndi mfumu ya ku Babulo, ndi Akasidi akuzinga inu, kunja kwa malinga, ndipo ndidzazisonkhanitsa pakati pa mudzi uwu.