Jeremiah 21:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ineyo mwiniwakene ndi mkono wanga wamphamvu, ndidzamenyana nanu nkhondo inuyo, ndili wopsa mtima, wokalipa ndi wokwiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ine mwini ndidzamenyana ndi inu ndi dzanja lotambasuka ndi mkono wamphamvu, m'mkwiyo, ndi m'kupsa mtima, ndi m'ukali waukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ineyo mwini wakene ndi mkono wotambasula ndi dzanja lamphamvu, ndidzachita nanu nkhondo ndili wokwiya, wokalipa ndi waukali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ine mwini ndidzamenyana ndi inu ndi dzanja lotambasuka ndi mkono wamphamvu, m'mkwiyo, ndi m'kupsya mtima, ndi m'ukali waukuru.