Jeremiah 21:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidzapititsa ku ukapolo Zedekiya mfumu ya ku Yuda pamodzi ndi nduna zake, ndi anthu otsala mumzindamu opulumuka ku mliri, ku njala ndi ku nkhondo. Ndidzaŵapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndiponso kwa adani ao amene akufuna kuŵapha. Adzaŵaphadi ndi lupanga, sadzaŵamvera chisoni kapena chifundo.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pambuyo pake, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ake, ndi anthu, ngakhale a m'mudzi uwu amene asiyidwa ndi chaola, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osachita chisoni, osachita chifundo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi anthu a mu mzinda muno amene adzapulumuke pa nthawi ya mliri, lupanga ndi njala kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi kwa adani awo amene ankafuna kuwapha. Iye adzawapha ndi lupanga. Sadzawachitira chifundo kapena kuwamvera chisoni kapenanso kuwakomera mtima.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pambuyo pace, ati Yehova, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi atumiki ace, ndi anthu, ngakhale a m'mudzi uwu amene asiyidwa ndi caola, ndi lupanga, ndi njala, m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, ndi m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la amene afuna moyo wao; ndipo adzawakantha ndi lupanga lakuthwa; osawaleka, osacita cisoni, osacita cifundo.