Jeremiah 21:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense wotsala mu mzinda uno adzafa ndi nkhondo, njala kapena mliri. Koma aliyense amene adzadzipereka kwa Ababiloni amene akuzingani ndi zithando zankhondo aja, ameneyo adzakhala ndi moyo, adzapulumuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye amene akhala m'mudzi uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola; koma iye amene atuluka, napandukira kwa Ababiloni akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wake udzapatsidwa kwa iye ngati chofunkha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzaphedwa ndi lupanga, njala kapena mliri. Koma aliyense amene apite kukadzipereka kwa Ababuloni amene akuzinganiwa adzakhala ndi moyo, adzapulumuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye amene akhala m'mudzi uwu adzafa ndi lupanga, ndi njala, ndi caola; koma iye amene aturuka, napandukira kwa Akasidi akuzinga inu, adzakhala ndi moyo, ndipo moyo wace udzapatsidwa kwa iye ngati cofunkha.