Jeremiah 22:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musailire mfumu, musaŵaimbire nyimbo malemuwo. Koma mulire amene wachotsedwa m'dziko lake chifukwa sadzabwereranso, sadzaliwonanso dziko lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamlirire wakufa, musachite maliro ake; koma mumliritse iye amene amuka, pakuti sadzabweranso, kapena kuonanso dziko la kwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musayilire mfumu Yosiya, musamuyimbire nyimbo womwalirayo; mʼmalo mwake, mulire kwambiri chifukwa cha Yehowahazi amene wapita ku ukapolo, chifukwa sadzabwereranso kapena kuonanso dziko lake lobadwira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamlirire wakufa, musacite maliro ace; koma mumliritse iye amene amuka, pakuti sadzabweranso, kapena kuonanso dziko la kwao.