Jeremiah 22:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja Salumu, mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, adaloŵa m'malo mwa atate ake pa mpando waufumu umene adausiya. Tsono ponena za amene uja Chauta akuti, “Iyeyo sadzabwereranso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m'malo mwake mwa Yosiya atate wake, amene anatuluka m'malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iliyonse;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti zimene Yehova akunena za Yehowahazi mwana wa Yosiya, amene anatenga mpando waufumu wa Yuda mʼmalo mwa abambo ake koma nʼkuwusiya ndi izi: “Iye sadzabwereranso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova atero za Salumu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene analamulira m'malo mwace mwa Yosiya atate wace, amene anaturuka m'malo muno: Sadzabweranso kuno nthawi iri yonse;