Jeremiah 22:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo, womanga zipinda zake monyenga, pogwiritsa ntchito anthu, koma osaŵapatsa malipiro a ntchito yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka iye amene amanga nyumba yake ndi chisalungamo, ndi zipinda zapamwamba ndi chosaweruza bwino; amene agwiritsa mnzake ntchito osamlipira, osampatsa mphotho yake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo, womanga zipinda zake zosanja monyenga, pogwiritsa ntchito abale ake mwathangata, osawapatsa malipiro a ntchito yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka iye amene amanga nyumba yace ndi cisalungamo, ndi zipinda zapamwamba ndi cosaweruza bwino; amene agwiritsa mnzace nchito osamlipira, osampatsa mphotho yace;