Jeremiah 22:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthuyo amanena kuti, ‘Ndidzadzimangira nyumba yaikulu, ya zipinda zam'mwamba zikuluzikulu, ndidzaikamo mawindo, ndi kukhomamo matabwa a mkungudza, ndipo ndidzaipaka utoto wofiira.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amene ati, Ndidzadzimangira ndekha nyumba yotakata ndi zipinda zapamwamba zazikulu, nadziboolera mazenera; navundikira chindwi lam'kati ndi mikungudza, naipaka ndi utoto wofiira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthuyo amati, ‘Ndidzadzimangira nyumba yayikulu ya zipinda zikuluzikulu zamʼmwamba.’ Kotero ndidzapanga mazenera akuluakulu, ndi kukhomamo matabwa a mkungudza ndi kukongoletsa ndi makaka ofiira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene ati, Ndidzadzimangira ndekha nyumba yotakata ndi zipinda zapamwamba zazikuru, nadziboolera mazenera; nabvundima chindwi lam'kati ndi mikungudza, naipaka ndi utoto wofiira.