Jeremiah 22:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi uganiza kuti ndiwe mfumu poti nyumba zako ndi zamkungudza? Ganiza za bambo wako: suja anali nazo zosoŵeka zonse? Suja ankaweruza molungama ndi mosakondera? Ndipo paja zonse zidamuyendera bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi udzakhala mfumu, chifukwa iwe uyesa kuposa ena ndi mikungudza? Kodi atate wako sanadye ndi kumwa, ndi kuweruza molungama? Kumeneko kunamkomera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi kukhala ndi nyumba ya mkungudza wambiri zingachititse iwe kukhala mfumu? Ganiza za abambo ako. Suja anali ndi zonse zakudya ndi zakumwa. Abambo ako ankaweruza molungama ndi mosakondera, ndipo zonse zinkawayendera bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi udzakhala mfumu, cifukwa iwe uyesa kuposa ena ndi mikungudza? Kodi atate wako sanadya ndi kumwa, ndi kuweruza molungama? kumeneko kunamkomera.