Jeremiah 22:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma iwe maganizo ako ndi mtima wako sizili penanso, zili pa phindu lonyenga, pa zopha anthu osalakwa, ndi pa zankhanza ndi zozunza ena.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosachimwa, ndi kusautsa, ndi zachiwawa, kuti uzichite.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Koma maso ako ndi mtima sizili penanso, koma zili pa phindu lachinyengo, pa zopha anthu osalakwa ndi pa kuzunza ndi pakulamulira mwankhanza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosacimwa, ndi kusautsa, ndi zaciwawa, kuti uzicite.