Jeremiah 22:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, akuti, “Sipadzakhala womulira munthu ameneyo kuti, ‘Kalanga ine, mbale wanga!’ Kapena kuti, ‘Kalanga ine, mlongo wanga!’ Sipadzakhala womulira kuti, ‘Kalanga ine, mbuye wanga!’ Kapena kuti, ‘Kalanga ine, mfumu yanga.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mwana wake wa Yosiya, mfumu ya Yuda: Sadzamlira iye, kuti, Kalanga ine mbale wanga! Kapena, Kalanga ine mlongo wanga! Sadzamlira, kuti, Kalanga ine mbuye! Kapena, Kalanga ine ulemerero wake!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Yehova ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda akuti, “Anthu sadzamulira maliro kapena kunena kuti, ‘Kalanga ine, mʼbale wanga! Kalanga ine mlongo wanga! Anthu ake sadzamulira maliro kuti, Kalanga ine, mbuye wathu! Taonani ulemerero wake wapita!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yehova atero za Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda: Sadzamlira iye, kuti, Kalanga ine mbale wanga! kapena, Kalanga ine mlongo wanga! Sadzamlira, kuti, Kalanga ine mbuye! kapena, Kalanga ine ulemerero wace!