Jeremiah 22:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Iwe mfumu ya ku Yuda, imva mau a Chauta. Imva iwe amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide, iweyo pamodzi ndi atumiki ako ndiponso anthu ako amene amaloŵera pa zipata izi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Imva mawu a Yehova, iwe mfumu ya ku Yuda, amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide; iwe, nduna zako pamodzi ndi anthu ako amene amalowera pa zipata izi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi.