Jeremiah 22:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, kwerani ku mapiri ku Lebanoni, mukalire mofuula kumeneko, mau anu amveke mpaka ku Basani. Mulire mofuula muli ku Abarimu, chifukwa onse amene munkaŵadalira aonongeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwera ku Lebanoni, nufuule; kweza mau ako m'Basani; nufuule m'Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, pitani ku mapiri a Lebanoni kuti mukalire mofuwula kumeneko, mawu anu akamveke mpaka ku Basani. Mulire mofuwula muli ku Abarimu chifukwa abwenzi ako onse awonongeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwera ku Lebano, nupfuule; kweza mau ako m'Basani; nupfuule m'Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha,