Jeremiah 22:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Pali Ine ndemwe, iwe Yehoyakini, mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ngakhale ukadakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikadakuvula nkukutaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pali Ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wake wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya pa dzanja langa lamanja, ndikadachotsa iwe kumeneko;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pali Ine wamoyo, akutero Yehova, ngakhale iwe, Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ukanakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikanakuvula nʼkukutaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pali ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wace wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya pa dzanja langa lamanja, ndikadacotsa iwe kumeneko;