Jeremiah 22:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakupereka kwa anthu ofuna kukupha, amene umaŵaopa, ndiye kuti kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni ndi anthu ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzakupereka iwe m'dzanja la iwo amene afuna moyo wako, m'dzanja la iwo amene uwaopa, m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, m'dzanja la Ababiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakupereka kwa amene akufuna kukupha, amene iwe umawaopa. Ndidzakupereka kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni ndi anthu ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzakupereka iwe m'dzanja la iwo amene afuna moyo wako, m'dzanja la iwo: amene uwaopa, m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, m'dzanja la Akasidi.