Jeremiah 22:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidati, “Kodi ndiye kuti Yehoyakiniyu wakhala ngati mbiya yonyozeka, yosweka, chinthu chimene anthu sakuchisamala? Nanga chifukwa chiyani iyeyu ndi ana ake akuŵachotsa ndi kuŵaponya ku dziko losadziŵika konse?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? Chifukwa chanji atulutsidwa iye, ndi mbeu zake, ndi kuponyedwa m'dziko limene salidziwa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Yehoyakini wakhala ngati mbiya yonyozeka, yosweka imene anthu sakuyifunanso? Kodi nʼchifukwa chake iye pamodzi ndi ana ake, achotsedwa nʼkutayidwa ku dziko limene iwo sakulidziwa?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? cifukwa canji aturutsidwa iye, ndi mbeu zace, ndi kuponyedwa m'dziko limene salidziwa?