Jeremiah 22:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Munthu ameneyu mumtenge ngati wopanda ana, munthu amene sadzakhoza pa moyo wake. Ndithu, palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake amene adzakhale pa mpando waufumu wa Davide ndi kudzalamuliranso Yuda.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Lembani munthu uyu wopanda ana, munthu wosaona phindu masiku ake; pakuti palibe munthu wa mbeu zake adzaona phindu, ndi kukhala pa mpando wachifumu wa Davide, ndi kulamuliranso m'Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Munthu ameneyu mumutenge ngati wopanda ana, munthu amene sadzakhala wochita bwino pamoyo wake wonse, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake zomwe zidzachita bwino. Palibe amene adzathe kukhala pa mpando waufumu wa Davide ndi kulamulira Yuda.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Lembani munthu uyu wopanda ana, munthu wosaona phindu masiku ace; pakuti palibe munthu wa mbeu zace adzaona phindu, ndi kukhala pa mpando wacifumu wa Davide, ndi kulamuliranso m'Yuda.