Jeremiah 22:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu, ukamadzamvera mau aŵa, ndiye kuti mafumu okhala pa mpando waufumu wa Davide adzapitirirabe kumalamulira. Azidzaloŵera pa zipata izi za ku nyumba ya mfumu, atakwera pa magaleta ndi pa akavalo, iwowo pamodzi ndi atumiki ao ndi anthu ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ngati mudzachitadi ichi pamenepo, padzalowa pa zipata za nyumba iyi mafumu okhala pa mpando wachifumu wa Davide, okwera m'magaleta ndi pa akavalo, iye, ndi atumiki ake, ndi anthu ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ngati udzamvera malamulo awa, ndiye kuti mafumu onse okhala pa mpando waufumu wa Davide azidzalowabe pa zipata za nyumba yaufumu ino, atakwera magaleta ndi akavalo, iwowo pamodzi ndi nduna zawo ndi anthu awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ngati mudzacitadi ici pamenepo, padzalowa pa zipata za nyumba iyi mafumu okhala pa mpando wacifumu wa Davide, okwera m'magareta ndi pa akavalo, iye, ndi atumiki ace, ndi anthu ace.