Jeremiah 22:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Naŵa mau a Chauta onena za nyumba ya mfumu ya ku Yuda: “Ngakhale iwe ndimakukonda ngati Giliyadi, kapena ngati nsonga ya phiri la Lebanoni, komabe ndidzakusandutsa chipululu, mzinda wopanda anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Giliyadi, ndi mutu wa Lebanoni; koma ndidzakuyesa iwe chipululu, ndi midzi yosakhalamo anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti zimene Yehova akunena za nyumba yaufumu ya mfumu ya ku Yuda ndi izi: “Ngakhale iwe uli ngati Giliyadi kwa Ine, ngati msonga ya phiri la Lebanoni, komabe ndidzakusandutsa chipululu, ngati mizinda yopanda anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Gileadi, ndi mutu wa Lebano; koma ndidzakuyesa iwe cipululu, ndi midzi yosakhalamo anthu.