Jeremiah 22:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Nchifukwa chakuti anthu akewo adasiya chipangano chimene adapangana ndi Chauta, Mulungu wao. Adayamba kupembedza milungu ina ndi kumaitumikira.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzayankha, Chifukwa anasiya pangano la Yehova Mulungu wao, ndi kugwadira milungu ina, ndi kuitumikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Chifukwa anasiya pangano limene anapangana ndi Yehova Mulungu wawo ndipo anapembedza ndi kutumikira milungu ina.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adza yankha, Cifukwa anasiya pangano la Yehova Mulungu wao, ndi kugwadira milungu yina, ndi kuitumikira.