Jeremiah 23:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko lino ladzaza ndi anthu achigololo. Chifukwa cha temberero la Chauta m'dziko mwagwa chilala, mabusa akuchipululu auma. Amene amangothamangira zoipa, amalimbikira kuchita zosalungama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko ladzaza ndi anthu achigololo; lili pansi pa matemberero. Dziko lasanduka chipululu ndipo msipu wawuma. Aneneri akuchita zoyipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti dziko ladzala ndi acigololo; pakuti cifukwa ca temberero dziko lilira, mabusa a kucipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siiri yabwino.