Jeremiah 23:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake njira zao zidzakhala zoterera. Adzaŵapirikitsira kumdima kumene akagwe. Ndidzaŵaonetsa ndoza pa nthaŵi ya chilango chao,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzachotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, chaka cha kulangidwa kwao, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake njira zawo zidzakhala zoterera; adzawapirikitsira ku mdima ndipo adzagwera kumeneko. Adzaona zosaona mʼnthawi ya chilango chawo,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzacotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, caka ca kulangidwa kwao, ati Yehova.