Jeremiah 23:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakati pa aneneri a ku Yerusalemunso ndaonapo chinthu choopsa kwambiri: amachita zigololo, amanena bodza, ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoipa, kotero kuti palibe amene amaleka machimo ake. Kwa Ine onsewo ali ngati anthu a ku Sodomu ndi Gomora.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu choopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ochita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zake; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo pakati pa aneneri a ku Yerusalemu ndaonapo chinthu choopsa kwambiri: amachita chigololo, amanena bodza ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoyipa. Choncho palibe amene amasiya zoyipa zake. Kwa Ine anthu onsewa ali ngati a ku Sodomu ndi Gomora.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona cinthu coopsetsa; acita cigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ocita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zace; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ace ngati Gomora.