Jeremiah 23:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa cha zimenezi, ponena za aneneri ameneŵa, Chauta akuti, “Ndidzaŵadyetsa dzoŵaŵa ndi kuŵamwetsa madzi azumu, chifukwa zoipa zimene zaŵanda m'dziko lonse zachokera kwa aneneri omweŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo chowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwatulukira kunka ku dziko lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ponena za aneneriwa Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndidzawadyetsa zakudya zowawa ndi kuwamwetsa madzi a ndulu, chifukwa uchimo umene wafalikira mʼdziko lonse ndi wochokera kwa aneneri a ku Yerusalemuwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace Yehova wa makamu atero za aneneri: Taonani, ndidzadyetsa iwo cowawa, ndidzamwetsa iwo madzi andulu; pakuti kwa aneneri a ku Yerusalemu kuipitsa kwaturukira kunka ku dziko lonse.