Jeremiah 23:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akuuza anthu kuti, “Musamvere zimene akunena aneneri, iwowo amakuloserani zonyenga. Zimene amakuuzani kuti akuziwona m'masomphenya ndi maganizo ao chabe, si zolankhula Chauta ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zachabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Musamvere zimene aneneri amenewa akulosera kwa inu; zomwe aloserazo nʼzachabechabe. Iwo akungoyankhula za masomphenya a mʼmitima mwawo basi, osati zochokera kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zacabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.