Jeremiah 23:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Saleka kuŵauza amene amandinyoza Ine kuti, ‘Zinthu zidzakuyenderani bwino.’ Ndipo amene amaumirira kutsata zofuna za mtima wao amaŵauza kuti, ‘Simudzaona vuto ai.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anena chinenere kwa iwo akundinyoza Ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wake amati, Palibe choipa chidzagwera inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo amapita ndi kumakawuza amene amandinyoza Ine kuti, ‘zinthu zidzakuyenderani bwino.’ Kwa iwo amene amawumirira kutsata zofuna za mitima yawo amakawawuza kuti, ‘palibe choyipa chimene chidzakugwereni.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anena cinenere kwa iwo akundinyoza Ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wace amati, Palibe coipa cidzagwera inu.