Jeremiah 23:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani mphepo yamkuntho yochokera kwa Chauta! Onani ukali wake woomba ngati namondwe, udzaomba pa mitu ya anthu oipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, chimphepo cha Yehova, kupsa mtima kwake, kwatuluka, inde chimphepo chozungulira; chidzagwa pamutu pa woipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani ukali wa Yehova uli ngati chimphepo chamkuntho, inde ngati namondwe. Ndipo adzakantha mitu ya anthu oyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, cimphepo ca Yehova, kupsa mtima kwace, kwaturuka, inde cimphepo cozungulira; cidzagwa pamutu pa woipa.