Jeremiah 23:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Chauta, Mulungu wa Israele, ponena za abusa oyang'anira anthu ake, akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga, simudazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa Israele, ponenera abusa amene adyetsa anthu anga: Mwabalalitsa zoweta zanga, ndi kuzipirikitsa, ndipo simunazizonda; taonani, ndidzakusenzani inu kuipa kwa ntchito zanu, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Yehova, Mulungu wa Israeli, ponena za abusa amene akuweta anthu anga akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga. Komanso simunazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, ponenera abusa amene adyetsa anthu anga: Mwabalalitsa zoweta zanga, ndi kuzipitikitsa, ndipo simunazizonda; taonani, ndidzakusenzani inu kuipa kwa nchito zanu, ati Yehova.