Jeremiah 23:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aneneri ameneŵa amakhulupirira kuti anthu anga adzandiiŵala akamamva zamalotozo, monga momwe makolo ao adaiŵalira dzina langa pomapembedza Baala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amene aganizira kuti adzaiwalitsa anthu anga dzina langa, ndi maloto ao amene anena munthu yense kwa mnansi wake, monga makolo ao anaiwala dzina limene ndimtcha nalo Baala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aneneriwa amakhulupirira kuti anthu anga adzayiwala mawu anga akamamva za maloto awo amene amayankhulana ngati mmene anachitira makolo awo popembedza Baala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amene aganizira kuti adzaiwalitsa anthu anga dzina langa, ndi maloto ao amene anena munthu yense kwa mnansi wace, monga makolo ao anaiwala dzina limene ndimcha nalo Baala.