Jeremiah 23:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikuŵakana aneneri amene amalota zabodza, namasimbira anthu anga ndi kumaŵasokeza ndi mabodza aowo. Sindidaŵatume ndine kapena kuŵalamula, ndipo sathandiza anthu mpang'ono pomwe,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, Ine ndidana ndi amene anenera maloto onama, ndi kuwafotokoza ndi kusokeretsa anthu anga ndi zonama zao, ndi matukutuku ao achabe; koma Ine sindinatuma iwo, sindinauza iwo; sadzapindulira konse anthu awa, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, Ine ndidana ndi amene anenera maloto onama, ndi kuwafotokoza ndi kusokeretsa anthu anga ndi zonama zao, ndi matukutuku ao acabe; koma Ine sindinatuma iwo, sindinauza iwo; sadzapindulira konse anthu awa, ati Yehova.