Jeremiah 23:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adauza Yeremiya kuti, “Anthu ameneŵa, kaya ndi mneneri, kaya ndi wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Chauta ukuti chiyani?’ Udzayankhe kuti, ‘Inuyo ndiye katundu wolemetsa Chauta, ndipo adzakutayani,’ akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anthu awa, kapena mneneri, kapena wansembe, adzakufunsa iwe, kuti, Katundu wa Yehova ndi chiyani? Pamenepo uziti kwa iwo, Katundu wanji? Ndidzakuchotsani inu, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Anthu awa, kapena mneneri, kapenanso wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Yehova ukuti chiyani?’ uwawuze kuti, ‘Inuyo ndinu katundu wolemetsa Yehova, ndipo adzakutayani.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anthu awa, kapena mneneri, kapena wansembe, adzakufunsa iwe, kuti, Katundu wa Yehova ndi ciani? pamenepo uziti kwa iwo, Katundu wanji? Ndidzakucotsani inu, ati Yehova.