Jeremiah 23:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma musanenanso kuti ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Chauta.’ Uthenga wa aliyense ndi mau a iye mwini, motero inuyo mudapotoza mau a Mulungu wamoyo, Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo katundu wa Yehova simudzatchulanso konse; pakuti mau a munthu adzakhala katundu wake; pakuti mwasokoneza mau a Mulungu wamoyo, Yehova wa makamu, Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma musanenenso kuti ‘nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ chifukwa mawu a munthu aliyense ndiwo uthenga wa iye mwini, kotero kuti inu mumakhotetsa mawu a Mulungu wamoyo, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo katundu wa Yehova simudzachulanso konse; pakuti mau a munthu adzakhala katundu wace; pakuti mwasokoneza mau a Mulungu wamoyo, Yehova wa makamu, Mulungu wathu.