Jeremiah 23:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo Ine mwini ndidzakunyamulani ngati katundu wolemetsa nkukutayani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndidakupatsani inu ndi makolo anu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake, taonani, ndidzakuiwalani inu konse, ndipo ndidzakuchotsani, ndi mudzi umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, ndidzauchotsa pamaso panga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndiye kuti Ine ndidzakunyamulani ngati katundu nʼkukuponyani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga, inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace, taonani, ndidzakuiwalani inu konse, ndipo ndidzakucotsani, ndi mudzi umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, ndidzaucotsa pamaso panga;