Jeremiah 23:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene anthu polumbira sazidzatinso, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraele ku dziko la Ejipito!’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake, taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, amene sadzatinso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israele kuwatulutsa m'dziko la Ejipito;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho, masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu sadzanenanso polumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku Igupto,’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace, taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, amene sadzatinso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kuwaturutsa m'dziko la Aigupto;