Jeremiah 23:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma azidzati, ‘Pali Chauta wamoyo, amene adatulutsa Aisraeli ku dziko lakumpoto, ndi ku maiko konse kumene adaŵabalalitsira.’ Ndithu ndidzaŵabwezera ku malo amene ndidapatsa makolo awo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma, Pali Yehova, amene anakweza ndi kutsogolera mbeu za nyumba ya Israele kuwatulutsa m'dziko la kumpoto, ndi kumaiko onse kumene ndinawapirikitsirako, ndipo adzakhala m'dziko lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa zidzukulu za Israeli ku dziko lakumpoto ndi ku mayiko konse kumene anawabalalitsira.’ Ndipo iwo adzawabweretsa ku dziko lawolawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma, Pali Yehova, amene anakweza ndi kutsogolera mbeu za nyumba ya Israyeli kuwaturutsa m'dziko la kumpoto, ndi ku maiko onse kumene ndinawapitikitsirako, ndipo adzakhala m'dziko lao.