Jeremiah 24:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adaatenga ukapolo Yehoyakini, mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, kuchoka naye ku Yerusalemu. Adaatenganso ukapolo akalonga onse a ku Yuda, anthu aluso ndi akatswiri enanso kupita nawo ku Babiloni. Nthaŵi imeneyo Chauta adandiwonetsa zinthu zina m'masomphenya, zinthuzo ndi izi: ndidaona madengu aŵiri a nkhuyu ali pakhomo pa Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, madengu awiri a nkhuyu oikidwa pakhomo pa Kachisi wa Yehova; Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni atachotsa am'nsinga Yekoniya mwana wake wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akulu a Yuda, ndi amisiri ndi achipala, kuwachotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda pamodzi ndi nduna zake, anthu aluso ndi akatswiri a ku Yuda ndi kupita nawo ku Babuloni. Pambuyo pake Yehova anandionetsa madengu awiri a nkhuyu atayikidwa pa khomo pa Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova anandionetsa ine, ndipo, taonani, mitanga iwiri ya nkhuyu yoikidwa pakhomo pa Kacisi wa Yehova; Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo atacotsa am'nsinga Yekoniya mwana wace wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, ndi akuru a Yuda, ndi amisiri ndi acipala, kuwacotsa ku Yerusalemu, nawatengera ku Babulo.