Jeremiah 24:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'dengu lina munali nkhuyu zabwino kwambiri, ngati nkhuyu zoyambirira kupsa. Koma m'dengu linalo munali nkhuyu zoipa kwambiri, zosatinso nkudyeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Dengu limodzi linali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kucha; ndipo dengu limodzi linali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼdengu limodzi munali nkhuyu zabwino kwambiri, ngati nkhuyu zoyambirira kucha. Mʼdengu linalo munali nkhuyu zoyipa kwambiri zosati nʼkudya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mtanga umodzi unali ndi nkhuyu zabwinobwino, ngati nkhuyu zoyamba kuca; ndipo mtanga umodzi unali ndi nkhuyu zoipaipa, zosadyeka, zinali zoipa.