Jeremiah 24:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adandifunsa kuti, “Iwe Yeremiya, kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona nkhuyu zabwino kwambiri, ndi zinanso zoipa kwambiri, zosatinso nkudyeka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa ine, Kodi uona chiyani, Yeremiya? Ndipo ndinati, Nkhuyu, nkhuyu zabwino, nzabwino ndithu; zoipazo nzoipa ndithu, zosadyeka poti nzoipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova anandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuona chiyani?” Ndinayankha kuti, “Ndikuona nkhuyu zabwino kwambiri ndi nkhuyu zoyipa zosati nʼkudya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa ine, Kodi uona ciani, Yeremiya? Ndipo ndinati, Nkhuyu, nkhuyu zabwino, nzabwino ndithu; zoipazo nzoipa ndithu, zosadyeka poti nzoipa.